CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | CHIVUMBULUTSO 20-22
“Taonani! Zinthu Zonse Zimene Ndikupanga N’zatsopano”
Yehova akulonjeza kuti adzapanga zinthu zonse kukhala zatsopano.
“Kumwamba kwatsopano”: Boma latsopano limene lidzakhazikitse chilungamo padziko lapansi
“Dziko lapansi latsopano”: Anthu amene amamvera ulamuliro wa Mulungu komanso kutsatira mfundo zake zolungama
“Zinthu zonse . . . n’zatsopano”: Tsiku lililonse tizidzakhala ndi zinthu zotichititsa kukhala osangalala ndipo tidzaiwaliratu mavuto onse amene tikukumana nawo panopa