Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • mwb20.03
  • Kodi Ndiitane Ndani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndiitane Ndani?
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mukukonzekera Chikumbutso?
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Yehova Amadalitsa Khama Lathu Loyesetsa Kuti Tipezeke pa Chikumbutso
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Kodi Mwakonzeka Kudzapezekapo pa Tsiku Lofunika Kwambiri pa Chaka?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
mwb20.03
M’bale akupereka kapepala koitanira ku Chikumbutso kwa munthu wina atakhala kukhitchini. Akazi awo akucheza kwinaku akuphika chakudya.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Ndiitane Ndani?

Chaka chilichonse timayesetsa kuitana anthu a m’gawo lathu kuti adzapezeke pa mwambo wa Chikumbutso. Ambiri mwa anthuwa sitiwadziwa. Komabe, tiyeneranso kumaitana anthu amene tikuwadziwa. Anthu amene amalandira kapepala kuchokera kwa anthu amene akuwadziwa, nthawi zambiri amabwera ku Chikumbutso. (yb08 11 ¶3; 14 ¶1) Kodi ndi anthu enanso ati omwe mungawaitane?

  • Achibale

  • Anzanu a kuntchito kapena a kusukulu

  • Oyandikana nawo nyumba

  • Maulendo anu obwereza, maphunziro anu komanso anthu omwe munkaphunzira nawo m’mbuyomo

Akulu akhozanso kuitana anthu omwe anafooka kuti abwere kumwambowu. Bwanji ngati munthu amene mumadziwana naye sakhala m’gawo la mpingo wanu? Mungamuthandize kudziwa nthawi ndi malo omwe kukachitikire mwambowo popita patsamba loyamba la webusaiti yathu pamene palembedwa kuti ZOKHUDZA IFEYO, n’kusankha pamene palembedwa kuti “Chikumbutso.” Pamene mukukonzekera Chikumbutso cha chaka chino, ganizirani za anthu amene mungawaitane kuti adzabwere pamwambowu.

Zithunzi: 1. M’bale akulalikira munthu pa nthawi yopuma kuntchito. 2. M’bale akuonetsa vidiyo munthu wogulitsa mulesitilanti.
    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani