Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • mwb20.08 4
  • Muzitamanda Yehova Pochita Upainiya

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzitamanda Yehova Pochita Upainiya
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
mwb20.08 4
M’bale akuwerengera munthu lemba kunyanja.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzitamanda Yehova Pochita Upainiya

Aisiraeli anali ndi zifukwa zomveka zotamandira Yehova. Anawatulutsa m’dziko la Iguputo komanso anawapulumutsa kwa asilikali a Farao. (Eks 15:1, 2) Yehova akupitirizabe kuchitira anthu ake zinthu zabwino. Ndiye kodi tingasonyeze bwanji kuyamikira zomwe amatichitira?​—Sl 116:12.

Njira imodzi ndi kuchita upainiya wothandiza kapena wokhazikika. Mungapemphe Yehova kuti akupatseni mphamvu komanso mtima wofuna kuchita upainiya. (Afi 2:13) Ambiri amayamba ndi kuchita upainiya wothandiza. Mungasankhe wa maola 30 kapena 50 m’miyezi ya March ndi April kapena pa nthawi imene woyang’anira dera akuchezera mpingo wanu. Pambuyo poona mmene mungasangalalire ndi upainiya wothandiza, mukhoza kukhala ndi mtima wofuna kuyamba upainiya wokhazikika. Ngakhale ena amene amagwira ntchito yolembedwa kapena ena amene amadwaladwala amakwanitsa kuchita upainiya wokhazikika. (mwb16.07 8) Kunena zoona, Yehova ndi woyenera kumutamanda ndipo tiyenera kuchita zonse zomwe tingathe.​—1Mb 16:25.

ONERANI VIDIYO YAKUTI ALONGO ATATU APACHIBALE A KU MONGOLIA, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Mbali ina ya vidiyo yakuti ‘Alongo Atatu Apachibale a ku Mongolia.’ Undraa, m’modzi mwa alongo omwe ndi apainiya, akukonzekera kukwera basi.

    Kodi alongo atatuwa anafunika kuthana ndi mavuto ati kuti ayambe upainiya?

  • Mbali ina ya vidiyo yakuti ‘Alongo Atatu Apachibale a ku Mongolia.’ Oyun, m’modzi mwa alongo omwe ndi apainiya, akugwira ntchito m’chipinda chodyera ku Beteli.

    Kodi anapeza madalitso otani?

  • Mbali ina ya vidiyo yakuti ‘Alongo Atatu Apachibale a ku Mongolia.’ Dorjkhand, m’modzi mwa alongo omwe ndi apainiya, akulalikira kwa munthu mu utumiki.

    Kodi anakhala ndi mwayi wochita mautumiki ena ati chifukwa choti ankachita upainiya wokhazikika?

  • Mbali ina ya vidiyo yakuti ‘Alongo Atatu Apachibale a ku Mongolia.’ Alongo atatu apachibale omwe ndi apainiya, limodzi ndi mayi awo.

    Kodi chitsanzo chawo chinathandiza bwanji anthu ena?

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani