CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 17-18
Amuna Odzichepetsa Amaphunzitsa Ena N’kumawapatsa Zochita
Abale odziwa zambiri amachita bwino akamaphunzitsa achinyamata kenako n’kuwapatsa zochita. Akamachita zimenezi amasonyeza kudzichepetsa, chikondi komanso kuti amaona zakutsogolo. Angachite bwanji zimenezi?
Sankhani abale amene akuoneka kuti akhoza kukwanitsa kusamalira maudindo ena
Afotokozereni momveka bwino zimene ayenera kuchita pogwira ntchitoyo
Ngati pangafunike ndalama, zipangizo, kapena zinthu zina kuti agwire bwino ntchitoyo, muziwapatsa zimenezo
Muziona mmene akugwirira ntchitoyo ndipo muziwasonyeza kuti mukuwadalira
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndi zochita ziti zimene ndingapereke kwa ena?’