CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 37-38
Maguwa Ansembe a Chihema Anali Ofunika pa Kulambira Koona
Maguwa ansembe a chihema anapangidwa potsatira malangizo a Yehova ndipo ankaimira zinthu zapadera.
Mofanana ndi kupereka zofukiza zosakanizidwa mwaluso, mapemphero ovomerezeka amene atumiki a Yehovafe timapereka kwa iye amamusangalatsa
Yehova ankalandira nsembe zimene zinkaperekedwa paguwa lansembe zopsereza. Guwali linali patsogolo pa malo opatulika m’bwalo la chihema ndipo zimenezi zimatikumbutsa kuti tiyenera kukhulupirira nsembe ya dipo ya Yesu kuti tisangalatse Mulungu.—Yoh 3:16-18; Ahe 10:5-10
Kodi tingakonzekere bwanji mapemphero athu kuti akhale ngati zofukiza kwa Mulungu?—Sl 141:2