CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Zochita za Ezara Zinachititsa Kuti Dzina la Yehova Lilemekezedwe
Ezara analola kuti mawu a Mulungu azimufika pamtima ndipo zimenezi zinakhudza zochita zake (Eza 7:10; w00-CN 10/1 14:8)
Ezara anathandiza anthu ena kuzindikira nzeru za Mulungu (Eza 7:25; si 75:5)
Chifukwa chakuti anadzichepetsa pamaso pa Mulungu, Ezara anali wotsimikiza mtima kuti Yehova amutsogolera komanso amuteteza (Eza 8:21-23 it-1 1158:4)
Nzeru yochokera kwa Mulungu imene Ezara anasonyeza inachititsa kuti mfumu imupatse maudindo akuluakulu. Mofanana ndi Ezara, khalidwe lathu lingachititse kuti dzina la Yehova lilemekezedwe.
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi anthu omwe si a Mboni amandilemekeza chifukwa chakuti ndimatsatira zimene Mulungu amafuna?’