CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Kusamvera Kumapweteketsa
Aisiraeli ena anakwatirana ndi anthu amene ankalambira mafano (Eza 9:1, 2; w06-CN 1/15 20:1)
Iwo sanatsatire malamulo a Mulungu omwe anali omveka bwino (Eza 9:10-12)
Kusamvera kwawo kunabweretsa mavuto ambiri kwa iwowo komanso mabanja awo (Eza 10:10, 11, 44)
Lamulo lililonse limene Yehova amatipatsa, limakhala lotithandiza. (w09-CN 10/1 10:6) Kumvera kumatithandiza kuti tipewe mavuto ambiri panopa, komanso tidzapeza madalitso osatha m’tsogolo.
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi kumvera Yehova kwandithandiza bwanji kuti ndipewe mavuto?’