NKHANI YOPHUNZIRA 35
NYIMBO NA. 123 Tizigonjera Mulungu Mokhulupirika
Kodi Akulu Angathandize Bwanji Anthu Amene Achotsedwa Mumpingo?
“Kumwamba kudzakhala chisangalalo chochuluka chifukwa cha munthu mmodzi wochimwa amene walapa kuposa cha anthu 99 olungama amene sakufunika kulapa.”—LUKA 15:7.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Munkhaniyi tiona chifukwa chake anthu ena amachotsedwa mumpingo komanso mmene akulu angawathandizire kuti alape n’cholinga choti akhalenso pa ubwenzi ndi Yehova.
1-2. (a) Kodi Yehova amaona bwanji anthu omwe amachita machimo koma osafuna kulapa? (b) Kodi Yehova amayembekezera kuti anthu omwe achita machimo achite chiyani?
YEHOVA si Mulungu wolekerera machimo. (Sal. 5:4-6) Iye amafuna kuti tizimvera mfundo zake zolungama zomwe zimapezeka m’Baibulo. N’zoona kuti Yehova sayembekezera kuti anthu omwe si angwiro azichita zinthu mosalakwitsa kalikonse. (Sal. 130:3, 4) Pa nthawi imodzimodziyo, iye salekerera ‘anthu osaopa Mulungu omwe amatenga kukoma mtima kwake kwakukulu kukhala chifukwa chochitira khalidwe lopanda manyazi.’ (Yuda 4) Ndipotu Baibulo limanena za ‘kuwonongedwa kwa anthu osaopa Mulungu’ pa nkhondo yake ya Aramagedo.—2 Pet. 3:7; Chiv. 16:16.
2 Koma Yehova safuna kuti aliyense adzawonongedwe. Monga mmene taonera munkhani za m’magaziniyi, Baibulo limafotokoza momveka bwino kuti Mulungu “akufuna kuti anthu onse alape.” (2 Pet. 3:9) Akulu amatsanzira Yehova akamathandiza moleza mtima anthu omwe achita tchimo kuti asinthe njira zawo n’kukhalanso naye pa ubwenzi. Koma nthawi zina anthu amene achita tchimo salapa. (Yes. 6:9) Ena amapitiriza kuchita zoipa ngakhale akulu atawathandiza mobwerezabwereza kuti alape. Ndiye kodi zikatero akulu ayenera kuchita chiyani?
“MʼCHOTSENI MUNTHU WOIPAYO”
3. (a) Kodi Baibulo limanena kuti akulu ayenera kuchita chiyani ndi munthu wosalapa? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti munthu amakhala kuti wasankha yekha kuti achotsedwe mumpingo?
3 Ngati munthu amene wachita tchimo sakulapa, akulu sangachitirenso mwina koma kutsatira malangizo a pa 1 Akorinto 5:13, akuti: “Mʼchotseni munthu woipayo pakati panu.” Apa zimakhala ngati wochimwayo wasankha kukumana ndi zotsatirapo za zochita zake ndipo amakhala akukolola zomwe iye anafesa. (Agal. 6:7) N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa iye amakhala kuti wakana kusintha ngakhale kuti akulu anamuthandiza mobwerezabwereza kuti alape. (2 Maf. 17:12-15) Zochita zake zimasonyeza kuti iye wasankha kukana kutsatira mfundo za Yehova.—Deut. 30:19, 20.
4. N’chifukwa chiyani pamaperekedwa chilengezo munthu wosalapa akachotsedwa mumpingo?
4 Munthu wochimwa yemwe sakulapa akachotsedwa, chilengezo chimaperekedwa kumpingo chonena kuti iye salinso wa Mboni za Yehova. Cholinga cha chilengezochi si kuchititsa manyazi munthuyo. Koma chimaperekedwa kuti anthu mumpingo atsatire malangizo a m’Malemba oti ‘asiye kugwirizana’ ndi munthuyo “ngakhalenso kudya naye.” (1 Akor. 5:9-11) Pali chifukwa chabwino chimene Mulungu anaperekera malangizowa. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Zofufumitsa zapangʼono zimafufumitsa mtanda wonse wa ufa wokandakanda.” (1 Akor. 5:6) Ngati munthu wosalapa sakuchotsedwa mumpingo zochita zake zingafooketse ena omwe akuyesetsa kutsatira mfundo zolungama za Yehova.—Miy. 13:20; 1 Akor. 15:33.
5. Kodi tizimuona bwanji munthu yemwe wachotsedwa mumpingo, nanga n’chifukwa chiyani?
5 Ndiye kodi tizimuona bwanji m’bale kapena mlongo yemwe wachotsedwa mumpingo? Ngakhale kuti sitiyenera kucheza naye, tizimuona ngati nkhosa yosochera. Nkhosa imene yachoka pagulu la zinzake ikhoza kubwereranso. Tizikumbukira kuti nkhosa yosocherayo inadzipereka kwa Yehova. N’zomvetsa chisoni kuti pa nthawiyi munthuyo amakhala kuti sakukwaniritsanso lonjezo la kudzipereka kwake ndipo izi zimakhala zoopsa. (Ezek. 18:31) Ngakhale zili choncho, Yehova amapitirizabe kusonyeza chifundo ndipo amayembekezera kuti munthuyo adzabwerera. Kodi akulu angathandize bwanji munthu wochimwa yemwe wachotsedwa mumpingo?
MMENE AKULU AMATHANDIZIRA ANTHU OMWE ACHOTSEDWA
6. Kodi akulu angachite chiyani kuti athandize munthu yemwe wachotsedwa mumpingo?
6 Munthu akachotsedwa mumpingo, kodi akulu amangomusiya osamuthandiza kuti abwererenso kwa Yehova? Ayi si choncho. Komiti ya akulu ikamamufotokozera munthu kuti wachotsedwa mumpingo, imamufotokozeranso zimene angachite kuti abwezeretsedwe. Koma si zokhazo, akulu amachitanso zambiri kuposa pamenepo. Nthawi zambiri iwo amamufotokozera kuti angakonde kudzakumana nayenso pakapita miyezi ingapo kuti aone ngati wasintha. Ngati munthuyo angavomere kudzakumana nayenso, pa nthawiyo akuluwo amamulimbikitsa mwachikondi kuti alape komanso kubwerera kwa Yehova. Ngakhale zitakhala kuti pa ulendowo munthuyo sanasonyeze kuti wasintha, akuluwo amayesetsa kukonza zoti adzakumane nayenso m’tsogolo.
7. Kodi akulu amasonyeza bwanji chifundo cha Yehova akamachita zinthu ndi munthu yemwe wachotsedwa mumpingo? (Yeremiya 3:12)
7 Akulu amayesetsa kutsanzira chifundo cha Yehova akamachita zinthu ndi munthu yemwe wachotsedwa mumpingo. Mwachitsanzo, Yehova sanadikire kuti Aisiraeli alape iye asanachitepo kanthu kuti awathandize. M’malomwake, iye ndi amene anayamba kuchitapo kanthu iwo asanayambe n’komwe kusonyeza kulapa. Monga tinaonera munkhani yachiwiri m’magaziniyi, Yehova anasonyeza chifundo pouza mneneri Hoseya kuti agwirizanenso ndi mkazi wake yemwe anali akuchitabe tchimo lalikulu. (Hos. 3:1; Mal. 3:7) Potsanzira Yehova, akulu amafunitsitsa kuthandiza munthu amene wachita tchimo kuti alape ndipo amachita zonse zomwe angathe kuti zisakhale zovuta kwa munthuyo kubwerera mumpingo.—Werengani Yeremiya 3:12.
8. Kodi fanizo la Yesu la mwana wolowerera likutithandiza bwanji kumvetsa chifundo cha Yehova? (Luka 15:7)
8 Kumbukirani fanizo la mwana wolowerera lomwe tinakambirana munkhani yachiwiri m’magaziniyi. Bambo a mwanayo atamuona akubwerera, “anamuthamangira nʼkumukumbatira ndipo anamukisa mwachikondi.” (Luka 15:20) Onani kuti bambowo sanadikire kuti mwanayo apemphe kaye kuti amukhululukire. M’malomwake, mofanana ndi bambo aliyense wachikondi, iwo ndi amene anayamba kuchitapo kanthu. Umu ndi mmenenso akulu amachitira ndi anthu amene asochera. Iwo amafuna kuti nkhosa zotayika zibwerere kwa Yehova. (Luka 15:22-24, 32) Kumwamba kumakhala chisangalalo chachikulu munthu wochimwa akabwerera, chimodzimodzinso padziko lapansi.—Werengani Luka 15:7.
9. Kodi Yehova amafuna kuti anthu amene achimwa achite chiyani?
9 Kuchokera pa zimene takambiranazi n’zoonekeratu kuti Yehova salekerera anthu osalapa. Komabe sawatayiratu, amafuna kuti iwo abwerere. Maganizo a Yehova kwa anthu ochimwa afotokozedwa pa Hoseya 14:4, pomwe amati: “Ndidzathetsa kusakhulupirika kwawo. Ndidzawakonda mwa kufuna kwanga, chifukwa ndasiya kuwakwiyira.” Mawu amenewa ayenera kuthandiza akulu kuti aziona chizindikiro chilichonse chosonyeza kuti munthu wayamba kulapa. Mawuwa akutsimikiziranso anthu amene anasiya Yehova kuti iye amawakonda ndipo akufuna kuti abwerere mwamsanga.
10-11. Kodi akulu angathandize bwanji munthu yemwe anachotsedwa mumpingo kalekale?
10 Nanga bwanji za anthu omwe anachotsedwa kalekale mumpingo, mwina zaka zambiri m’mbuyomo? Anthu oterewa mwina amakhala kuti sakuchitanso machimo omwe anachititsa kuti achotsedwe. Nthawi zinanso sakumbukira n’komwe chomwe chinachititsa kuti achotsedwe. Kaya papita nthawi yaitali bwanji, akulu adzayesa kufufuza komanso kuyendera anthu amenewa. Pa maulendo amenewo akulu akhoza kupemphera nawo komanso kuwalimbikitsa mwachikondi kuti abwerere mumpingo. Ngati munthuyo wakhala kunja kwa zaka zambiri, n’zosachita kufunsa kuti angakhale wofooka mwauzimu. Choncho akasonyeza kuti akufuna kubwerera, akuluwo angakonze zoti munthu wina aziphunzira naye Baibulo ngakhale kuti sanabwezeretsedwe. Pa zochitika zonsezi, akulu ndi amene ayenera kukonza zoti munthuyo aziphunzira Baibulo.
11 Akulu ayenera kutsanzira chifundo cha Yehova poyesetsa kuthandiza anthu ambiri kudziwa kuti mwayi udakalipo woti akhoza kubwerera kwa Yehova. Ngati munthu wochimwa walapa ndipo wasiya zoipa zomwe amachita, ayenera kubwezeretsedwa mwamsanga.—2 Akor. 2:6-8.
12. (a) Kodi ndi pa nthawi iti pomwe akulu ayenera kukhala osamala kwambiri? (b) N’chifukwa chiyani sitiyenera kuganiza kuti anthu omwe anachita machimo enaake sangachitiridwe chifundo ndi Yehova? (Onaninso mawu a m’munsi)
12 Nthawi zina akulu ayenera kuchita zinthu mosamala kwambiri asanabwezeretse munthu mumpingo. Mwachitsanzo, ngati munthuyo anachitira nkhanza mwana, kuyamba mpatuko kapenanso anachita kukonza zoti athetse banja lake, akulu ayenera kutsimikizira kuti walapadi. (Mal. 2:14; 2 Tim. 3:6) Iwo ayenera kuteteza abale ndi alongo mumpingo. Pa nthawi imodzimodziyo, tizizindikira kuti Yehova ndi wokonzeka kulandira munthu yemwe walapa kuchokera pansi pa mtima ndipo wasiya zoipa zomwe ankachita. Ngakhale kuti akulu ayenera kusamala ndi anthu amene anachitira chinyengo anzawo, iwo sayenera kuganiza kuti pali ochimwa ena omwe sangachitiridwe chifundo ndi Yehova.a—1 Pet. 2:10.
ZIMENE MPINGO UNGACHITE
13. Kodi timatani munthu akadzudzulidwa, nanga timatani munthu akachotsedwa mumpingo?
13 Mogwirizana ndi nkhani yapita ija, nthawi zina chilengezo chimaperekedwa chonena kuti munthu wadzudzulidwa. Zikatero tingathe kupitiriza kuchita naye zinthu podziwa kuti analapa ndipo anasiya zoipa zimene ankachita. (1 Tim. 5:20) Iye amakhalabe mbali ya mpingo ndipo amafunika kulimbikitsidwa pocheza ndi Akhristu anzake. (Aheb. 10:24, 25) Koma umu si mmene zimakhalira munthu akachotsedwa mumpingo. Timasiya kugwirizana naye “ngakhale kudya naye munthu wotereyu.”—1 Akor. 5:11.
14. Kodi Akhristu angagwiritse ntchito bwanji chikumbumtima chawo ngati munthu wina wochotsedwa mumpingo? (Onaninso chithunzi.)
14 Kodi zimene takambiranazi zikutanthauza kuti tizinyalanyaziratu munthu amene wachotsedwa mumpingo? Ayi. N’zoona kuti sitingamacheze naye. Koma Akhristu akhoza kugwiritsa ntchito chikumbumtima chawo posankha kuti aitanire munthu amene wachotsedwa kumisonkhano makamaka ngati wochotsedwayo ndi wachibale kapena anali mnzawo. Ndiye kodi akapezeka pamisonkhano tizitani? M’mbuyomu sitinkamupatsa moni munthu wotereyu. Koma pamenepanso Mkhristu aliyense akhoza kuchita zinthu mogwirizana ndi chikumbumtima chake. Ena angasankhe kumupatsa moni kapena kumulandira kumisonkhano. Komabe sitingalankhule naye kwambiri kapena kucheza naye.
Ngati munthu wachotsedwa mumpingo, Akhristu angagwiritse ntchito chikumbumtima chawo posankha kumuitanira kumisonkhano kapena kumupatsa moni wachidule akafika kumisonkhanoyo (Onani ndime 14)
15. Kodi lemba la 2 Yohane 9-11 limanena za anthu amene achita machimo ati? (Onaninso bokosi lakuti “Kodi Yohane ndi Paulo Ankanena za Machimo Ofanana?”)
15 Ena akhoza kufunsa kuti, ‘Kodi si paja Baibulo limanena kuti munthu akapereka moni kwa wochotsedwa amakhala ngati akuchita nawo ntchito zake zoipazo?’ (Werengani 2 Yohane 9-11.) Nkhani yonse palembali imasonyeza kuti malangizowa ankanena za anthu ampatuko kapena amene amalimbikitsa makhalidwe oipa. (Chiv. 2:20) Choncho ngati munthu amalimbikitsa mpatuko kapena makhalidwe oipa, akulu sangakonze zomuyendera. Komabe pamakhala chiyembekezo chakuti iye angadzasinthe maganizo. Podikira nthawi imene adzasintheyo, munthu wotereyu sitimupatsa moni kapena kumuitanira kumisonkhano.
TIZITSANZIRA CHIFUNDO CHA YEHOVA
16-17. (a) Kodi Yehova amafuna kuti ochimwa achite chiyani? (Ezekieli 18:32) (b) Kodi akulu angasonyeze bwanji kuti akugwira ntchito ndi Yehova pothandiza anthu omwe achita machimo?
16 Kodi takambirana chiyani munkhani 5 zimenezi? Yehova safuna kuti aliyense adzawonongedwe. (Werengani Ezekieli 18:32.) Koma amafuna kuti anthu ochimwa abwerere kwa iye. (2 Akor. 5:20) N’chifukwa chake kwa nthawi yaitali komanso mobwerezabwereza Yehova wakhala akuuza anthu ake monga gulu komanso aliyense payekhapayekha kuti alape ndi kubwerera kwa iye. Akulu amagwira ntchito ndi Yehova pothandiza anthu omwe achita machimo kuti alape.—Aroma 2:4; 1 Akor. 3:9.
17 Kumwamba kumakhala chisangalalo chachikulu wochimwa akalapa. Atate wathu wakumwamba Yehova amasangalalanso kwambiri nkhosa yosochera ikabwerera mumpingo. Timakonda kwambiri Yehova tikaganizira za chifundo chake komanso kukoma mtima kwake kwakukulu.—Luka 1:78.
NYIMBO NA. 111 Tili Ndi Zifukwa Zambiri Zokhalira Osangalala
a Baibulo limanena kuti anthu ena sadzakhululukidwa. Anthu amenewa amakhala kuti asankha kuti nthawi zonse azitsutsana ndi Mulungu. Ndi Yehova kapena Yesu yekha amene amadziwa kuti munthu ndi wosayenera kumukhululukira.—Maliko 3:29; Aheb. 10:26, 27.