NKHANI YOPHUNZIRA 17
NYIMBO NA. 99 Abale Ambirimbiri
Sitili Tokha
“Ndikuthandiza.”—YES. 41:10.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Munkhaniyi tikambirana njira 4 zimene Yehova amatithandizira.
1-2. (a) N’chifukwa chiyani sitinganene kuti timakhala tokha tikakumana ndi mayesero? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
TIKAKUMANA ndi mayesero aakulu, tikhoza kumakhala ngati tili tokhatokha m’kaboti kakang’ono panyanja yomwe pali mafunde. Koma sikuti timakhala tokha. Atate wathu wakumwamba amadziwa mavuto amene tikukumana nawo ndipo amatilonjeza kuti atithandiza. Yehova amatsimikizira mtumiki wake aliyense kuti: “Ndikuthandiza.”—Yes. 41:10.
2 Munkhaniyi tikambirana mmene Yehova amatithandizira m’njira 4 izi: (1) potitsogolera, (2) potipatsa zinthu zofunika, (3) potiteteza, komanso (4) potilimbikitsa. Yehova amatilonjeza kuti kaya tikumana ndi mavuto otani, iye sadzatiiwala. Iye sangatisiye, choncho sitili tokha.
YEHOVA AMATITSOGOLERA
3-4. Kodi Yehova amatitsogolera bwanji? (Salimo 48:14)
3 Werengani Salimo 48:14. Yehova sayembekezera kuti tizidzitsogolera tokha. Ndiye kodi amatsogolera bwanji anthu ake masiku ano? Njira imodzi imene amachitira zimenezi ndi kudzera m’Baibulo. (Sal. 119:105) Mawu ake amatithandiza kuti tizisankha bwino zochita komanso tizikhala ndi makhalidwe omwe angachititse kuti tizisangalala panopa komanso tidzapeze moyo wosatha m’tsogolo.a Mwachitsanzo, amatiphunzitsa kuti tisamasunge mkwiyo, tizikhala oona mtima pa zinthu zonse komanso tizikondana kuchokera mumtima. (Sal. 37:8; Aheb. 13:18; 1 Pet. 1:22) Tikamasonyeza makhalidwewa timakhala mwamuna kapena mkazi wabwino, makolo abwino komanso timagwirizana ndi anzathu.
4 Yehova anaika m’Mawu ake nkhani za anthu amene anakumana ndi mayesero amene timakumana nawo komanso ankamva ngati mmene ifeyo timamvera. (1 Akor. 10:13; Yak. 5:17) Tikamawerenga nkhani zimenezi komanso kugwiritsa ntchito zimene tikuphunzira, timapindula m’njira ziwiri. Choyamba, timazindikira kuti sitili tokha chifukwa anthu ena anakumananso ndi mavuto ngati omwewo n’kuwapirira bwinobwino. (1 Pet. 5:9) Chachiwiri, timaphunzira zimene tingachite kuti tipirire mavutowo.—Aroma 15:4.
5. Kodi Yehova amagwiritsa ntchito ndani potitsogolera pa njira yopita ku moyo?
5 Yehova amatitsogoleranso kudzera mwa Akhristu anzathu.b Mwachitsanzo, oyang’anira madera amayendera mipingo kuti atilimbikitse. Nkhani zawo zimalimbitsa chikhulupiriro chathu komanso kutithandiza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. (Mac. 15:40–16:5) Akulu mumpingo amachitanso chidwi ndi wofalitsa aliyense. (1 Pet. 5:2, 3) Makolo amaphunzitsa ana awo kuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, akhale oganiza bwino komanso akhale ndi makhalidwe abwino. (Miy. 22:6) Komanso alongo olimba mwauzimu amathandiza alongo achitsikana powapatsa chitsanzo chabwino, malangizo othandiza komanso kuwalimbikitsa.—Tito 2:3-5.
6. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tizipindula ndi malangizo a Yehova?
6 Yehova wachita mbali yake potipatsa malangizo ofunika. Kodi tingasonyeze bwanji kuyamikira zimene watichitira? Lemba la Miyambo 3:5, 6 limati: “Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usamadalire luso lako lomvetsa zinthu.” Tikatero, “iye adzawongola njira zathu,” kutanthauza kuti adzatithandiza kupewa mavuto ambiri n’kumakhala osangalala. Timayamikira kwambiri kuti Yehova amatikonda komanso kutipatsa malangizo othandiza.—Sal. 32:8.
YEHOVA AMATIPATSA ZIMENE TIMAFUNIKIRA
7. Kodi Yehova amatipatsa zofunika m’njira ziti? (Afilipi 4:19)
7 Werengani Afilipi 4:19. Kuwonjezera pa kutitsogolera mwauzimu, Yehova amadalitsa khama lathu kuti tipeze chakudya, zovala ndi pogona. (Mat. 6:33; 2 Ates. 3:12) Mwachibadwa anthufe timadera nkhawa mmene tingapezere zinthu zofunika koma Yehova amatilimbikitsa kuti tisamadere nkhawa kwambiri zinthu zimenezi. (Mat. 6:25) Tikutero chifukwa chakuti Atate wathu sangasiye atumiki ake amene akuvutika. (Mat. 6:8; Aheb. 13:5) Tiyenera kukhulupirira zimene anatilonjeza kuti azitithandiza kupeza zofunika pa moyo.
8. Kodi Yehova anathandiza bwanji Davide?
8 Taganizirani mmene Yehova anathandizira Davide. Pa zaka zimene Davide ndi anthu ake ankakhala moyo wothawathawa, Yehova ankawapatsa zimene ankafunikira. Ataganizira mmene Yehova anamusamalirira pa zaka zimenezo, Davide analemba kuti: “Ndinali mwana ndipo tsopano ndakula, koma sindinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa, kapena ana ake akupemphapempha chakudya.” (Sal. 37:25) Mwina inunso mwaonapo pa moyo wanu Yehova akupereka zofunika kwa atumiki ake okhulupirika.
9. Kodi Yehova amathandiza bwanji anthu masiku ano pakachitika ngozi inayake? (Onaninso zithunzi.)
9 Yehova amaperekanso kwa atumiki ake zofunika pa nthawi imene kwachitika ngozi inayake. Mwachitsanzo kutagwa njala ku Yerusalemu m’nthawi ya atumwi, Akhristu a m’madera osiyanasiyana anatumiza zinthu zofunika kwa abale ndi alongo awo omwe anakhudzidwa. (Mac. 11:27-30; Aroma 15:25, 26) Izi ndi zimene anthu a Yehova amachitanso masiku ano. Kukachitika ngozi inayake, Yehova amalimbikitsa anthu ake kuti athandize anzawo powapatsa zinthu monga chakudya, madzi, zovala ndiponso mankhwala. Magulu a zomangamanga amakonza nyumba za abale komanso Nyumba za Ufumu zimene zawonongeka. Anthu a Yehova amagwiritsa ntchito mfundo za m’Malemba pothandiza komanso kulimbikitsa anzawo amene katundu wawo wawonongeka kapena amene aferedwa.c
Kodi Yehova amatilimbikitsa bwanji pakachitika ngozi inayake? (Onani ndime 9)e
10-11. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Borys?
10 Yehova amathandizanso anthu omwe sanayambe kumutumikira kuti azipeza zinthu zofunika. Nafenso timayesetsa kukomera mtima anthu amene satumikira Yehova. (Agal. 6:10) Zimenezi zimathandiza kuti tiwalalikire. Chitsanzo ndi mphunzitsi wamkulu pasukulu ina ya ku Ukraine dzina lake Borys. Iye si wa Mboni za Yehova koma nthawi zonse ankakomera mtima komanso kulemekeza ana a sukulu a Mboni. Pa nthawi ina pomwe ankafuna kuthawira kudera lina chifukwa cha nkhondo abale athu anamuthandiza. Kenako Borys anapezeka pa Mwambo Wokumbukira Imfa ya Khristu. Pokumbukira zimene zinachitika pa nthawiyo Borys ananena kuti: “A Mboniwo ankachita nane zinthu mokoma mtima komanso kundisamalira. Ndimathokoza kwambiri a Mboni za Yehova.”
11 Ifenso tingatsanzire chifundo cha Atate wathu wakumwamba posonyeza chikondi kwa anthu amene akuvutika, ngakhale amene satumikira Yehova. (Luka 6:31, 36) Timakhulupirira kuti tikamakonda anthu ena zingawathandize kuti adzakhale ophunzira a Khristu. (1 Pet. 2:12) Kaya anthuwo adzakhala atumiki a Yehova kapena ayi, ifeyo timapeza chimwemwe chimene chimabwera chifukwa chopatsa.—Mac. 20:35.
YEHOVA AMATITETEZA
12. Kodi Yehova analonjeza kuti aziteteza bwanji anthu ake monga gulu? (Salimo 91:1, 2, 14)
12 Werengani Salimo 91:1, 2, 14. Yehova watilonjeza kuti azititeteza mwauzimu. Iye sangalole kuti Satana asokoneze kulambira koona. (Yoh. 17:15) Sitikukayikira kuti “chisautso chachikulu” chikadzayamba, Yehova adzakwaniritsa zimene analonjeza kuti adzatithandiza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba komanso adzatipulumutsa.—Chiv. 7:9, 14.
13. Kodi Yehova amatiteteza bwanji aliyense payekha?
13 Kodi Yehova amateteza bwanji munthu aliyense payekha? Yehova amagwiritsa ntchito Malemba potithandiza kudziwa zoyenera ndi zolakwika. (Aheb. 5:14) Tikamatsatira mfundo zopezeka m’Mawu ake, iye amatiteteza ku zinthu zimene zingativulaze komanso zimene zingawononge chikhulupiriro chathu. (Sal. 91:4) Yehova amatitetezanso kudzera mu mpingo. (Yes. 32:1, 2) Tikamagwirizana ndi anthu amene amakonda Yehova komanso kutsatira mfundo zake, timalimbikitsidwa ndiponso timapewa zoipa.—Miy. 13:20.
14. (a) N’chifukwa chiyani Yehova satiteteza ku mayesero ena? (b) Kodi lemba la Salimo 9:10 limatitsimikizira chiyani? (Onaninso mawu a m’munsi.)
14 Nthawi zina Yehova ankateteza atumiki ake akale kuti asavulazidwe kapena kuphedwa. Koma sikuti ankachita zimenezo nthawi zonse. Ifenso timatha kukumana ndi “zinthu zosayembekezereka.” (Mlal. 9:11) Nthawi zina Yehova wakhala akulola atumiki ake kuzunzidwa kapenanso kuphedwa pofuna kusonyeza kuti Satana ndi wabodza. (Yobu 2:4-6; Mat. 23:34) Zimenezi zingachitikenso masiku ano. Ngakhale kuti Yehova sangatichotsere mayesero, timakhulupirira kuti iye sangasiye anthu omwe amamukonda.d—Sal. 9:10.
YEHOVA AMATILIMBIKITSA
15. Kodi timalimbikitsidwa bwanji ndi pemphero, Mawu a Mulungu komanso Akhristu anzathu? (2 Akorinto 1:3, 4)
15 Werengani 2 Akorinto 1:3, 4. Akhristufe nthawi zina timamva chisoni kapenanso kukhala ndi nkhawa. Mwina panopa mukukumana ndi vuto linalake lomwe likukuchititsani kuti muzidzimva ngati muli nokhanokha. Dziwani kuti Yehova akudziwa mmene mukumvera. Iye amamvetsa mmene tikumvera ndipo “amatitonthoza pa mayesero athu onse.” Kodi amatitonthoza bwanji? Tikapemphera kwa Yehova mochonderera, iye amatipatsa “mtendere [wake] umene anthu sangathe kuumvetsa.” (Afil. 4:6, 7) Timalimbikitsidwanso tikawerenga Baibulo n’kumva mawu a Yehova. Kudzera m’Mawu ake ouziridwawa, iye amatitsimikizira kuti amatikonda, amatiuza zimene tingachite kuti tikhale anzeru komanso amatipatsa chiyembekezo. Tikakhala pamisonkhano timalimbikitsidwanso tikamacheza ndi Akhristu anzathu komanso kutonthozedwa ndi mfundo za m’Malemba.
16. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Nathan ndi Priscilla?
16 Chitsanzo cha Nathan ndi Priscilla, omwe amakhala ku United States, chimatitsimikizira kuti Yehova amatilimbikitsa komanso kutitonthoza pogwiritsa ntchito Mawu ake. Zaka zingapo m’mbuyomu, iwo anaganiza zosamukira kudera lina komwe kunkafunika olalikira ambiri. Nathan anati: “Tinkakhulupirira kuti Yehova adzatidalitsa pa utumiki wathuwu.” Koma iwo atangofika kuderalo anakumana ndi mavuto a zachuma komanso matenda. Kenako anabwerera kunyumba kwawo ndipo anapitirizabe kukumana ndi mavuto a zachuma. Nathan anati: “Ndinkadabwa kuti n’chifukwa chiyani Mulungu sanatidalitse ngati mmene tinkayembekezerera. Ndinayamba kuganiza kuti mwina ndalakwitsa zinazake.” Koma kenako Nathan ndi Priscilla anazindikira kuti Mulungu sanawasiye pa nthawi ya mavutoyi. Nathan anati: “Pa nthawi yovutayi, Baibulo linali ngati mnzathu yemwe ankatilimbikitsa komanso kutipatsa malangizo. Kuganizira mmene Yehova anatithandizira kuti tipirire, m’malo momaganizira mayesero amene tinkakumana nawowo, kunatithandiza kuti tikhale okonzeka kukumana ndi mayesero ena m’tsogolo tili ndi chikhulupiriro cholimba.”
17. Kodi mlongo wina dzina lake Helga analimbikitsidwa bwanji? (Onaninso chithunzi.)
17 Kodi abale ndi alongo amatilimbikitsa bwanji? Taganizirani zimene zinachitikira Helga yemwe amakhala ku Hungary. Kwa zaka zambiri, iye anakumana ndi mavuto ambiri omwe ankachititsa kuti azisowa pogwira n’kumadziona ngati wosafunika. Koma akaganizira zimene zinachitika amaona kuti Yehova anamuthandiza kudzera mwa abale ndi alongo. Iye analemba kuti: “Yehova wakhala akundithandiza akaona kuti ndafooka chifukwa cha ntchito, kusamalira mwana wanga wodwala kapenanso mayesero ena. Pa zaka 30 zonsezi iye wakhala akukwaniritsa lonjezo lake lakuti azindilimbikitsa. Nthawi zambiri amandilimbikitsa kudzera mwa abale ndi alongo omwe amandilankhula mokoma mtima komanso mondiganizira. Ndakhala ndikulandira pa nthawi yoyenera mameseji, makadi kapenanso mawu olimbikitsa.”
Kodi Yehova angatigwiritse ntchito bwanji potonthoza ena? (Onani ndime 17)
18. Kodi tingalimbikitse bwanji anthu ena?
18 Ifenso tikhoza kutsanzira Mulungu polimbikitsa anthu ena. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tiyenera kuwamvetsera moleza mtima, kuwalankhula mawu olimbikitsa komanso kuwapatsa zimene akufunika. (Miy. 3:27) Tiziyesetsa kulimbikitsa anthu onse amene akuvutika ngakhale amene sakutumikira Mulungu panopa. Ngati aneba athu akudwala, ali ndi chisoni kapena ali ndi nkhawa, timawayendera, kuwamvetsera komanso kukambirana nawo malemba olimbikitsa. Tikamatsanzira Yehova, yemwe ndi “Mulungu amene amatitonthoza pa vuto lililonse,” timathandiza Akhristu anzathu kupirira mayesero komanso timafewetsa mitima ya anthu ena kuti ayambe kulambira koona.—Mat. 5:16.
YEHOVA AZITITHANDIZA NTHAWI ZONSE
19. Kodi Yehova amatichitira chiyani, nanga tingamutsanzire bwanji?
19 Yehova amaganizira anthu amene amamukonda. Iye samatisiya tikakumana ndi mavuto. Amasamalira atumiki ake okhulupirika ngati mmene kholo lachikondi limasamalira mwana wake. Amatitsogolera, kutiteteza, kutilimbikitsa komanso ndi alokutipatsa zimene timafunikira. Timatsanzira Atate wathu wakumwamba tikamathandiza komanso kulimbikitsa anthu ena omwe akumana ndi mavuto. Kaya tikumane ndi mavuto otani, tisamakayikire kuti Yehova ali nafe. Paja iye analonjeza kuti: “Usachite mantha, chifukwa ndili ndi iwe.” (Yes. 41:10) Mawu amenewa amatilimbitsa mtima ndipo timadziwa kuti sitili tokha.
NYIMBO NA. 100 Alandireni Bwino
a Onani nkhani yakuti “Zosankha Zanu Zizilemekeza Mulungu” mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 2011.
b Onani ndime 11-14 munkhani yakuti “Pitirizani Kutsatira Malangizo a Yehova” mu Nsanja ya Olonda ya February 2024.
c Mungapeze nkhani zatsopano polemba pamalo ofufuzira pa jw.org mawu akuti “zogwa mwadzidzidzi.”
d Onani nkhani yakuti “Yehova ndi Wokhulupirika” mu Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya April 2019.
e MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Abale ndi alongo a ku Malawi akulandira thandizo komanso kulimbikitsidwa mwauzimu pambuyo poti kwachitika ngozi.