NKHANI YOPHUNZIRA 18
NYIMBO NA. 65 Pita Patsogolo
Achinyamata, Muzitsanzira Maliko ndi Timoteyo
“Ubwerenso ndi Maliko chifukwa amandithandiza pa utumiki wanga.”—2 TIM. 4:11.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Tiona mmene chitsanzo cha Maliko ndi Timoteyo chingalimbikitsire achinyamata kuti akhale ndi makhalidwe amene angawathandize kuti azitumikira ena mumpingo.
1-2. Kodi ndi mavuto ati omwe akanalepheretsa Maliko ndi Timoteyo kuti azichita zambiri potumikira ena?
KODI ndinu wachinyamata ndipo mumafuna muzichita zambiri potumikira Yehova komanso abale ndi alongo anu mumpingo? N’zosakayikitsa kuti mumafuna kuchita zimenezo. N’zosangalatsa kuti pali achinyamata ambiri amene amafunitsitsa kutumikira ena. (Sal. 110:3) Koma pali zinthu zina zimene zingakulepheretseni kuchita zimenezi. Mwachitsanzo, kodi mumaopa kuwonjezera utumiki wanu chifukwa cha mantha? Kodi munakanapo utumiki winawake chifukwa chodzikayikira? Dziwani kuti si inu nokha amene munamvapo choncho.
2 Maliko ndi Timoteyo anakumananso ndi mavuto amenewa. Koma iwo sanalolere kuti mantha kapena kusadziwa zambiri kuwalepheretse kutumikira ena. Zikuoneka kuti Maliko ankakhala ndi mayi ake m’nyumba yabwino pa nthawi imene mtumwi Paulo ndi Baranaba anamupempha kuti ayende nawo pa ulendo woyamba wa umishonale. (Mac. 12:12, 13, 25) Koma Maliko analolera kusiya zonsezo kuti awonjezere utumiki wake. Choyamba anapita ku Antiokeya. Kenako anapita kumadera akutali ndi Paulo ndi Baranaba. (Mac. 13:1-5) Zikuoneka kuti nayenso Timoteyo ankakhala ndi makolo ake pamene Paulo anamupempha kuti azigwira nawo ntchito yolalikira. Popeza Timoteyo sankadziwa zambiri komanso anali wamng’ono, akanatha kukana chifukwa chodzikayikira. (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 16:10, 11 ndi 1 Timoteyo 4:12) Koma iye anavomera ndipo anapeza madalitso ambiri.—Mac. 16:3-5.
3. (a) Kodi tikudziwa bwanji kuti Paulo ankayamikira Maliko ndi Timoteyo? (2 Timoteyo 4:6, 9, 11) (Onaninso zithunzi.) (b) Kodi tikambirana mafunso ati munkhaniyi?
3 Maliko ndi Timoteyo anaphunzira zambiri ndipo anali okonzeka kusamalira maudindo akuluakulu ali achinyamata. Paulo ankayamikira kwambiri achinyamatawa moti atatsala pang’ono kuphedwa anawaitanitsa kuti abwere. (Werengani 2 Timoteyo 4:6, 9, 11.) Kodi Maliko ndi Timoteyo anali ndi makhalidwe ati omwe anachititsa kuti Paulo aziwakonda? Kodi abale achinyamata angawatsanzire bwanji? Nanga kodi angapindule bwanji ndi malangizo amene anapereka?
Paulo ankakonda Maliko ndi Timoteyo chifukwa iwo anali okonzeka kusamalira maudindo akuluakulu ali achinyamata (Onani ndime 3)b
KHALANI NDI MTIMA WOFUNA KUTUMIKIRA NGATI MALIKO
4-5. Kodi Maliko anasonyeza bwanji kuti anali wofunitsitsa kutumikira ena?
4 Magazini ina inanena kuti kutumikira ena kumatanthauza kuthandiza ena “mwakhama komanso mosalekeza.” Maliko anapereka chitsanzo chabwino pa nkhaniyi. Iye ayenera kuti anakhumudwa Paulo atakana kumutenga pa ulendo wake wachiwiri. (Mac. 15:37, 38) Koma izi sizinafooketse Maliko mpaka kusiya kutumikira abale ndi alongo ake.
5 Maliko anavomera kukatumikira ndi msuweni wake Baranaba. Patapita zaka 11, Maliko anali mmodzi wa anthu amene anathandiza Paulo pamene anamangidwa koyamba ku Roma. (Filim. 23, 24) Ndipotu Paulo anayamikira zimene Maliko anamuchitira moti anafika ponena kuti “amandilimbikitsa kwambiri.”—Akol. 4:10, 11.
6. Kodi Maliko anapindula bwanji chifukwa chogwirizana ndi abale olimba mwauzimu? (Onani mawu a m’munsi.)
6 Maliko anadalitsidwa chifukwa chogwirizana ndi Akhristu olimba mwauzimu. Atakhala ndi Paulo kwa kanthawi ku Roma, Maliko anapita kukatumikira ku Babulo ndi mtumwi Petulo. Iwo ankagwirizana kwambiri moti Petulo ankamutchula kuti “mwana wanga Maliko.” (1 Pet. 5:13) Pamene ankatumikira limodzi, Petulo ayenera kuti ankamuuza zinthu zambiri zochititsa chidwi zokhudza moyo ndi utumiki wa Yesu. Pambuyo pake Maliko analemba zimenezi mu uthenga wake wabwino.a
7. Kodi Seung-Woo anatsanzira bwanji Maliko? (Onaninso chithunzi.)
7 Maliko anapitirizabe kuchita khama pa utumiki wake moti ankagwirizanabe ndi Akhristu olimba mwauzimu. Kodi mungatsanzire bwanji Maliko? Ngati mwalephera kupeza mwayi winawake wa utumiki, muzikhala oleza mtima ndipo muzipeza njira zina zomwe mungatumikirire Yehova ndi abale ndi alongo anu. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi m’bale wina dzina lake Seung-Woo yemwe pano ndi mkulu. Iye ali wamng’ono ankadziyerekezera ndi abale ena a msinkhu wake. Ena mwa abalewo anali atapatsidwa utumiki. Seung-Woo ankaona kuti sakuwerengedwa ndipo anafotokozera maganizo akewo abale olimba mwauzimu. Mkulu wina anamulangiza kuti azingochita zimene angathe pothandiza ena ngakhale kuti zabwino zimene angachite sizingaonekere kwa anthu ena. Malangizo amenewa anamuthandiza kuti azithandiza achikulire komanso anthu ena omwe ankavutika pa nkhani ya mayendedwe popita kumisonkhano. Poganizira zimene zinachitika, iye anati: “Tsopano ndamvetsa tanthauzo la kutumikira ena ndi mtima wonse. Panopa ndimakhala wosangalala chifukwa chothandiza anthu ena.”
Kodi achinyamata amapindula bwanji akamagwirizana ndi abale olimba mwauzimu? (Onani ndime 7)
MUZIGANIZIRA ENA NGATI TIMOTEYO
8. N’chifukwa chiyani Paulo anasankha Timoteyo kuti aziyenda naye? (Afilipi 2:19-22)
8 Paulo ankafunika anthu olimba mtima oti apite nawo kumizinda imene anazunzidwa. Poyamba anasankha Sila yemwe anali Mkhristu wodziwa zambiri. (Mac. 15:22, 40) Kenako anasankhanso Timoteyo kuti ayende naye. Kodi n’chiyani chimene chinamuchititsa kuti asankhe Timoteyo? Chinthu chimodzi n’chakuti iye anali ndi mbiri yabwino. (Mac. 16:1, 2) Komanso Timoteyo ankakonda anthu kuchokera pansi pa mtima.—Werengani Afilipi 2:19-22.
9. Kodi Timoteyo anasonyeza bwanji kuti ankakonda kwambiri abale ndi alongo?
9 Atangoyamba kutumikira ndi Paulo, Timoteyo anasonyeza kuti ankakonda kwambiri anthu kuposa mmene ankadzikondera. Pa chifukwa chimenechi Paulo anamudalira n’kumusiya ku Bereya kuti alimbikitse ophunzira atsopano. (Mac. 17:13, 14) Pa nthawiyo Timoteyo ayenera kuti anaphunzira zambiri kwa Sila yemwenso anatsala komweko. Kenako Paulo anatumiza Timoteyo kumzinda wa Tesalonika kuti akalimbikitse Akhristu kumeneko. (1 Ates. 3:2) Choncho kwa zaka 15 kapena kuposa, Timoteyo anaphunzira ‘kulira ndi amene akulira’ ndipo ankasonyeza chifundo anthu amene akuvutika. (Aroma 12:15; 2 Tim. 1:4) Kodi Akhristu achinyamata angatsanzire bwanji Timoteyo?
10. Kodi n’chiyani chinathandiza Woo Jae kuti azichita chidwi ndi ena?
10 M’bale wina dzina lake Woo Jae anaphunzira kuchita chidwi ndi anthu ena. Ali wachinyamata, iye ankavutika kucheza ndi abale ndi alongo omwe ndi aakulu kuposa iyeyo. Choncho akakhala ku Nyumba ya Ufumu ankangowapatsa moni n’kuchokapo. Mkulu wina anamuuza kuti akhoza kumacheza ndi abale ndi alongo poyamba n’kuwayamikira. Anamuuzanso kuti aziganizira zimene anthu angachite nazo chidwi. Iye anatsatira malangizo amenewa. Panopa Woo Jae ndi mkulu ndipo anati: “Panopa sindimavutika kucheza ndi anthu a misinkhu yonse. Ndimasangalala chifukwa panopa ndimatha kudziwa mmene zinthu zili pa moyo wa ena komanso zimene zikuwadetsa nkhawa. Izi zachititsa kuti ndizitha kuthandiza Akhristu anzanga.”
11. Kodi achinyamata angatani kuti azichita chidwi ndi ena mumpingo? (Onaninso chithunzi.)
11 Inunso achinyamata mungathe kuphunzira kuti muzichita chidwi ndi ena. Mukakhala pamisonkhano muzichita chidwi ndi anthu a misinkhu ndi zikhalidwe zonse. Muziwafunsa mmene zinthu zilili pa moyo wawo ndipo muziwamvetsera. Mukatero mudzadziwa zimene mungachite kuti muwathandize. Mwachitsanzo, mungadziwe kuti banja lina la achikulire likufunika kulithandiza mmene lingagwiritsire ntchito pulogalamu ya JW Library. Kapenanso mungadziwe kuti alibe woyenda naye mu utumiki. Kodi mungawathandize kudziwa mmene angagwiritsire ntchito chipangizo chawo chamakono, kapenanso kukonza zoti muyende nawo pokalalikira? Mukamayesetsa kuthandiza anthu ena, mudzapereka chitsanzo chabwino kwa onse.
Abale achinyamata angathandize mumpingo m’njira zambiri (Onani ndime 11)
MALANGIZO A PAULO ANGAKUTHANDIZENI
12. Kodi achinyamata angatani kuti malangizo amene Paulo analembera Timoteyo aziwathandiza?
12 Paulo anapatsa malangizo Timoteyo omwe akanamuthandiza pa moyo ndi utumiki wake. (1 Tim. 1:18; 2 Tim. 4:5) Ngati ndinu wachinyamata, kodi malangizo amenewo angakuthandizeni bwanji? Werengani makalata awiri a Paulo opita kwa Timoteyo ndipo muziwerenga ngati alembera inuyo, kenako onani mmene mungagwiritsire ntchito malangizo ake. Tiyeni tione malangizo ena omwe ali m’makalatawo.
13. Kodi munthu angalimbitse bwanji ubwenzi wake ndi Yehova?
13 “Uzidziphunzitsa nʼcholinga choti ukhalebe wodzipereka kwa Mulungu.” (1 Tim. 4:7b) Kodi kudzipereka kwa Mulungu kumatanthauza chiyani? Mawu amenewa amatanthauza kukonda kwambiri Yehova komanso kufunitsitsa kumusangalatsa. Anthufe sitimabadwa ndi khalidwe limeneli choncho timachita kufunika kuliphunzira. Mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti ‘kudziphunzitsa’ amafotokoza zimene ochita masewera ankachita pokonzekera. Anthu amenewa ankafunika kukhala odziletsa. Ifenso tiyenera kukhala odziletsa kuti tikhale ndi makhalidwe amene angachititse kuti tikhale pa ubwenzi ndi Yehova.
14. Kodi cholinga chathu tikamawerenga Baibulo chiyenera kukhala chiyani? Perekani chitsanzo.
14 Mukamaphunzira Baibulo, cholinga chanu chizikhala kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova. Mwachitsanzo, kodi mungaphunzire chiyani pa zimene zinachitika Yesu atakumana ndi wolamulira wina wachinyamata. (Maliko 10:17-22) Wachinyamatayo ankakhulupirira kuti Yesu ndi Mesiya koma analibe chikhulupiriro cholimba moti n’kukhala wotsatira wake. Ngakhale zinali choncho, Yesu “anamukonda” kwambiri. Yesu analankhula mokoma mtima ndi wachinyamatayo. Mosakayikira, Yesu ankafuna kuti wachinyamatayo asankhe zinthu mwanzeru. Apa Yesu anasonyezanso mmene Yehova ankakondera wachinyamatayo. (Yoh. 14:9) Mukamaganizira nkhaniyi komanso mmene zinthu zilili pa moyo wanu, muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ndingatani kuti ndikhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova n’kumachita zambiri potumikira ena?’
15. N’chifukwa chiyani achinyamata ayenera kupereka chitsanzo chabwino? Perekani chitsanzo. (1 Timoteyo 4:12, 13)
15 “Ukhale chitsanzo kwa okhulupirika.” (Werengani 1 Timoteyo 4:12, 13.) Paulo analimbikitsa Timoteyo kuti akulitse luso lowerenga ndi kuphunzitsa. Koma anamulimbikitsanso kuti akhale ndi makhalidwe monga chikondi, chikhulupiriro komanso kuti akhale woyera. Anamulimbikitsa zimenezi chifukwa anthu amaona kwambiri zochita kusiyana ndi zolankhula. Tiyerekeze kuti mwapatsidwa nkhani yolimbikitsa anthu kuti akhale akhama pa ntchito yolalikira. Mukhoza kuikamba momasuka ngati inuyo mumachita khama pa ntchitoyi. Chitsanzo chanu chinganene zambiri kuposa zimene mungalankhule.—1 Tim. 3:13.
16. (a) Mogwirizana ndi 1 Timoteyo 4:12, kodi achinyamata ayenera kukhala chitsanzo chabwino pa mbali 5 ziti? (b) Kodi wachinyamata angapereke bwanji chitsanzo chabwino ‘pa zimene amalankhula’?
16 Pa 1 Timoteyo 4:12, Paulo anatchula kuti achinyamata ayenera kupereka chitsanzo chabwino m’mbali 5. Mukamaphunzira Baibulo panokha, mungachite bwino kuganizira mbali 5 zimenezi. Tiyerekeze kuti mukufuna kukhala chitsanzo chabwino ‘pa zimene mumalankhula.’ Muyenera kuganizira mmene mungalankhulire zinthu zolimbikitsa anthu ena. Ngati mumakhala ndi makolo anu, muyenera kumawayamikira pafupipafupi chifukwa cha zimene amakuchitirani. Misonkhano ikatha mungauze munthu wina amene anali ndi nkhani kapena chitsanzo zimene wachita bwino. Muziyesetsanso kuyankha m’mawu anuanu pamisonkhano. Mukamachita khama kuti mukhale chitsanzo chabwino pa zimene mumalankhula, mudzasonyeza kuti mukupita patsogolo.—1 Tim. 4:15.
17. Kodi n’chiyani chingathandize wachinyamata kuti akwaniritse zolinga zake zauzimu? (2 Timoteyo 2:22)
17 “Thawa zilakolako za unyamata, koma tsatira chilungamo.” (Werengani 2 Timoteyo 2:22.) Paulo analimbikitsa Timoteyo kuti azipewa kulakalaka zinthu zimene zikanasokoneza zolinga zake zauzimu kapenanso kuwononga ubwenzi wake ndi Yehova. Palinso zinthu zina zomwe si zolakwika koma zikhoza kukuwonongerani nthawi yolimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova. Mwachitsanzo, kodi mumakhala nthawi yaitali bwanji mukuchita masewera, kufufuza zinthu pa intaneti kapena kusewera magemu a pa kompyuta? Kodi mungagwiritse ntchito nthawi imeneyo potumikira Yehova komanso anthu ena? Mwina mungadzipereke kuti mugwire nawo ntchito yokonza Nyumba ya Ufumu kapena kuchita ulaliki wa pashelefu. Mosakayikira, zimenezi zingakuthandizeni kuti mupeze anzanu atsopano omwe angakuthandizeni kukwaniritsa zolinga zanu zauzimu.
TIMADALITSIDWA TIKAMATUMIKIRA ANTHU ENA
18. N’chiyani chikusonyeza kuti Maliko ndi Timoteyo anadalitsidwa kwambiri?
18 Maliko ndi Timoteyo ankadzipereka kuti atumikire anthu ena ndipo anadalitsidwa kwambiri. (Mac. 20:35) Maliko anayenda m’madera osiyanasiyana kuti akatumikire anthu ena. Iye analembanso buku la Uthenga Wabwino wonena za moyo ndi utumiki wa Yesu. Timoteyo anathandiza Paulo poyambitsa mipingo komanso kulimbikitsa abale ndi alongo ake. N’zodziwikiratu kuti Yehova anasangalala ndi mtima wodzipereka umene Timoteyo anali nawo.
19. N’chifukwa chiyani achinyamata ayenera kutsatira malangizo amene Paulo analembera Timoteyo, nanga pangakhale zotsatira zotani?
19 Makalata amene Paulo analembera Timoteyo amasonyeza kuti ankamukonda kwambiri. Makalata ouziridwawa amasonyezanso kuti Yehova amakonda achinyamata. Iye amafuna kuti zinthu zizikuyenderani bwino. Choncho muzitsatira ndi mtima wonse malangizo amene Paulo anapereka ndipo muzifunitsitsa kuchita zambiri potumikira ena. Mukatero zinthu zidzakuyenderani bwino panopa ndipo ‘mudzagwira mwamphamvu moyo weniweni’ umene ukubwerawo.—1 Tim. 6:18, 19.
NYIMBO NA. 80 “Talawani Ndipo Muona Kuti Yehova Ndi Wabwino”
a Nthawi zambiri Petulo ankasonyeza mmene akumvera, choncho ayenera kuti anafotokozera Maliko mmene Yesu ankamvera pa zochitika zosiyanasiyana.—Maliko 3:5; 7:34; 8:12.
b MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Maliko akuthandiza Paulo ndi Baranaba pa ulendo wawo wa umishonale. Timoteyo akuyendera mpingo kuti alimbikitse abale.