Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • w25.05 101
  • Muzikonzekeretsa Mtima Wanu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzikonzekeretsa Mtima Wanu
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Nkhani Yofanana
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​—Muzithandiza Ophunzira Anu Kuti Azikonzekera
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Mfundo Zothandiza Pophunzira
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Ezara Ankaphunzitsa Chilamulo cha Mulungu
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Musasiye Kukonda Yehova—Mat. 22:37.
    Pulogalamu ya Msonkhano Wadera ya 2016-2017
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
w25.05 101

MFUNDO ZOTHANDIZA POPHUNZIRA

Muzikonzekeretsa Mtima Wanu

Tikamaphunzira Baibulo timafuna kuti maganizo a Yehova akhazikike mumtima mwathu. Ezara anatipatsa chitsanzo pomwe “anakonzekeretsa mtima wake kuti aphunzire Chilamulo cha Yehova.” (Ezara 7:10) Kodi tingamutsanzire bwanji pa nkhaniyi?

Muzipemphera. Nthawi zonse musanayambe kuphunzira muzipemphera. Muzimupempha Yehova kuti akuthandizeni kumvetsa komanso kugwiritsa ntchito zimene mukufuna kuphunzirazo.—Sal. 119:​18, 34.

Muzikhala odzichepetsa. Mulungu amabisira choonadi anthu onyada omwe amadalira nzeru zawo. (Luka 10:21) Komanso musamafufuze n’cholinga chofuna kugometsa anthu ena ndi zomwe mukudziwa. Modzichepetsa, muzisintha kaganizidwe kanu mukaona kuti sikakugwirizana ndi kaganizidwe ka Mulungu.

Muzimvetsera nyimbo ya Ufumu. Nyimbo zili ndi mphamvu zotha kukonzekeretsa mtima wathu tikamafuna kulambira. Choncho kumvetsera nyimbo ya Ufumu musanayambe kuphunzira kungakuthandizeni kukonzekeretsa mtima wanu.

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani