Mawu a M'munsi
a Mwachitsanzo, anthu Ayoruba ku Nigeria ali ndi chikhulupiriro chamwambo cha kubadwanso kwa moyo. Motero pamene mayi afedwa mwana, pamakhala chisoni chachikulu koma kwa nyengo yaifupi, pakuti monga momwe mwambi wa Ayoruba umanenera: “Madzi ndiwo atayikira. Chikho sichinasweke.” Malinga ndi kunena kwa Ayoruba, izi zimatanthauza kuti chikho chokhala ndi madziwo, mayiyo, akhoza kubala mwana wina—mwinamwake mwa kubadwanso kwa moyo wa wakufayo. Mboni za Yehova sizimatsatira miyambo iliyonse yozikidwa pa malaulo ochokera m’malingaliro onama a moyo wosafa ndi kubadwanso kwa moyo, imene ilibe maziko m’Baibulo.—Mlaliki 9:5, 10; Ezekieli 18:4, 20.