Mawu a M'munsi
e Anthu ena amati Paulo ankanena zimene zinamuchitikira pa nthawiyi pamene anauza anthu a ku Korinto kuti: “Tinalibe chiyembekezo choti tikhala ndi moyo.” (2 Akor. 1:8) Komabe, n’kutheka kuti ankatanthauza zinthu zina zoopsa zimene zinamuchitikira pa nthawi ina. Pamene Paulo analemba kuti “ndinamenyana ndi zilombo ku Efeso,” ayenera kuti ankatanthauza kuti anamenyanadi ndi zilombo zolusa m’bwalo la masewera, kapenanso ankatanthauza anthu amene ankamutsutsa. (1 Akor. 15:32) N’kutheka kuti mawu amenewa angatanthauze zilombo zenizeni kapena zophiphiritsa.