Mawu a M'munsi
c Nkhani imeneyi ikusonyeza zinthu ziwiri zopanda ulemu zimene ana a Eli ankachita. Chilamulo chinaneneratu zigawo za nyama yoperekedwa nsembe zimene ansembe ankayenera kudya. (Deut. 18:3) Koma ansembe oipawa anayamba kuchita zawozawo. Iwo ankauza anthu owathandizira kuti azipisa ndi chifoloko chachikulu m’miphika ya nyama ili pamoto n’kusankha nthuli iliyonse imene akufuna. Komanso anthu akabweretsa nsembe zawo kuchihema kuti azipereke paguwa la nsembe, ansembewo ankachititsa owathandizira awo kuchitira chipongwe anthu odzapereka nsembewo. Iwo ankakakamiza anthuwo kuti aziwapatsa nyama yosaphika, ngakhale asanapereke mafuta a nyamayo ngati nsembe kwa Yehova.—Lev. 3:3-5; 1 Sam. 2:13-17.