Mawu a M'munsi
b Zikuoneka kuti Davide ankaona kuti kuteteza anthu a m’derali ndiponso ziweto zawo kunali kutumikira Yehova Mulungu. Masiku amenewo, Yehova ankafuna kuti mbadwa za Abulahamu, Isake ndi Yakobo zizikhala m’derali. Choncho kuteteza anthu a m’derali ndiponso ziweto zawo unali utumiki wopatulika.