Mawu a M'munsi
a Mfumu inalola kuti Ayuda amenyenso nkhondo tsiku lotsatira n’cholinga chakuti amalize kugonjetsa adani awo. (Esitere 9:12-14) Mpaka pano, chaka chilichonse Ayuda amakumbukirabe kupambana kumeneku m’mwezi wa Adara womwe ndi chakumapeto kwa mwezi wa February ndi kumayambiriro kwa March. Mwambowu umatchedwa Purimu ndipo anaupatsa dzina limeneli potengera dzina la maere amene Hamani anachita aja.