Mawu a M'munsi
c Anthu othawa kwawo akafika, akulu ayenera kutsatira mwamsanga malangizo opezeka pamutu 8, ndime 30 m’buku lakuti Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova. Akulu angapemphe ofesi ya nthambi ya m’dziko lawo kuti iwathandize kuti azilumikizana ndi mipingo ya m’dziko lina. Akhoza kuchita zimenezi pogwiritsa ntchito webusaiti ya jw.org. Angachite bwinonso kufufuza mwanzeru kuti adziwe mpingo umene anthuwo akuchokera komanso moyo wawo wauzimu.