Mawu a M'munsi
a Anthu ambiri sazindikira kuti mawu opezeka pa Yohane 7:53 ndi 8:1-11 sapezeka m’mipukutu yoyambirira ya Baibulo koma anthu anachita kuwonjezera. Anthu ena akawerenga nkhaniyi amaganiza kuti munthu amene sanachimwepo ndi amene ayenera kuweruza munthu amene wachita chigololo. Koma lamulo limene Yehova anapereka kwa Aisiraeli linali lakuti: “Mwamuna akapezeka akugona ndi mkazi wa mwiniwake, mwamuna ndi mkaziyo, onsewo azifera pamodzi.”—Deut. 22:22.