Mawu a M'munsi
b Masiku ano anthu ambiri amakonda kutumizirana mauthenga, zithunzi, kapena mavidiyo olaula. Malinga ndi zinthu zimene anthu akutumizirana, akhoza kukumana ndi komiti yoweruza. Nthawi zina, ana amene amatumizirana zinthu zoterezi amatha kuimbidwa mlandu ndi boma. Kuti mumve zambiri, pitani pawebusaiti ya jw.org pa nkhani yakuti “Zimene Achinyamata Amadzifunsa—Kodi Ndiyenera Kudziwa Zotani pa Nkhani Yotumizirana Mameseji ndi Zinthu Zina Zolaula?” (Onani pamene alemba kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ACHINYAMATA.) Mutha kuonanso nkhani yakuti “Kukambirana ndi Mwana Wanu Nkhani Yotumizirana Zinthu Zolaula” mu Galamukani! ya November 2013, tsamba 4-5.