Mawu a M'munsi
c Akulu alibe udindo wopanga malamulo pa nkhani ya zosangalatsa. Mkhristu aliyense ayenera kugwiritsa ntchito chikumbumtima chake chophunzitsidwa Baibulo posankha nkhani zoti awerenge, mavidiyo oti aonere kapena masewera oti achite. Anthu omwe ndi mitu ya mabanja ayenera kuonetsetsa kuti banja lawo likutsatira mfundo za m’Baibulo posankha zosangalatsa.—Onani nkhani ya pa jw.org® yakuti, “Kodi Muli ndi Lamulo Loletsa Mavidiyo Ena, Mabuku Ena Ndiponso Nyimbo Zina?” Pitani pamene alemba kuti ZOKHUDZA IFEYO > MAFUNSO OFUNSIDWA KAWIRIKAWIRI.