Mawu a M'munsi
c MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: CHOYAMBA: M’bale ndi mlongo afika pa Nyumba ya Ufumu. Tingati ali pamalo amene mzimu wa Yehova umapezeka chifukwa choti asonkhana ndi Akhristu anzawo. CHACHIWIRI: Iwo akonzekera misonkhano n’cholinga choti ayankhe. Timafunika kutsatira mfundo ziwiri ngati zimenezi pochita zinthu zina zimene zatchulidwa munkhaniyi: kuphunzira Mawu a Mulungu, kugwira ntchito yolalikira ndiponso kupemphera kwa Yehova.