Mawu a M'munsi
c MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Pamsonkhano wa bungwe la akulu, m’bale wachikulire yemwe amachititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda wapemphedwa kuti aphunzitse mkulu wachinyamata kuti azichititsa phunzirolo. Ngakhale kuti m’bale wachikulireyo amakonda kwambiri udindo wakewu, akuchita zinthu mogwirizana ndi zimene akulu asankha pouza m’bale wachinyamatayo zimene zingamuthandize kuti azichititsa bwino komanso akumuyamikira.