Mawu a M'munsi
a Mbali yomaliza ya chaputala 15 cha buku la 1 Akorinto ikufotokoza za kuuka kwa akufa, makamaka kokhudza Akhristu odzozedwa. Koma zimene Paulo analemba m’chaputalachi n’zofunikanso kwa a nkhosa zina. Munkhaniyi, tiona mmene kuyembekezera kuti akufa adzauka kuyenera kukhudzira moyo wathu panopa komanso kutithandiza kuti tidzakhale osangalala m’tsogolo.