Mawu a M'munsi
a Yesu ananena kuti ophunzira ake adzadziwika ngati amasonyezana chikondi pakati pawo. Tonsefe timayesetsa kuti tizisonyeza ena chikondi. Tiyenera kuphunzira kukonda abale ndi alongo athu mmene timakondera achibale athu enieni. Nkhani ino itithandiza kukulitsa komanso kupitirizabe kusonyeza chikondi chenicheni kwa abale ndi alongo athu mumpingo.