Mawu a M'munsi
b MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Apolisi amanga m’bale kunyumba kwake. Mkazi ndi mwana wake akuona pamene iwo akumutenga. Pamene m’baleyo ali kundende, abale ndi alongo abwera kunyumba kwake ndipo akuchita kulambira kwa pabanja ndi mkazi ndi mwana wake. Mayi ndi mwana wakeyo akumapemphera kwa Yehova pafupipafupi kuti awapatse mphamvu zotha kupirira mayesero amene akumana nawo. Yehova wawapatsa mtendere wamumtima ndipo wawathandiza kukhala olimba mtima. Zotsatira zake n’zakuti chikhulupiriro chawo chalimba kwambiri, zomwe zawathandiza kuti azipirira mosangalala.