Mawu a M'munsi
c MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Onani mmene kuphunzira Baibulo kungathandizire munthu kusintha moyo wake: Poyamba munthuyu akuona kuti moyo wake ulibe cholinga chifukwa sadziwa Yehova. Kenako wakumana ndi a Mboni omwe akulalikira ndipo wavomera kuti aziphunzira Baibulo. Zimene waphunzira zamuthandiza kuti adzipereke kwa Yehova ndipo akubatizidwa. M’kupita kwa nthawi nayenso akuthandiza ena kuti akhale ophunzira a Yesu. Pamapeto pake onse akusangalala m’Paradaiso.