Mawu a M'munsi
a Tonsefe timakumana ndi mavuto. Padakali pano palibe njira yothetsera mavutowa, moti timangofunika kuwapirira. Koma si ife tokha amene tifunika kupirira. Nayenso Yehova akupirira zinthu zambiri. Munkhaniyi tikambirana zinthu zokwana 9 zimene akupirira. Tionanso zinthu zabwino zimene zakhala zikuchitika chifukwa chakuti Yehova wakhala akupirira komanso mmene chitsanzo chake chingatithandizire.