Mawu a M'munsi
a Mofanana ndi timing’alu tomwe tingachititse kuti mphika wadothi ukhale wosalimba, mtima wampikisano ungachititse kuti mpingo ugawikane. Ngati mpingo si wolimba ndipo anthu sakugwirizana, sungakhale malo a mtendere olambiriramo Mulungu. Munkhaniyi tikambirana chifukwa chake tiyenera kupewa mtima wampikisano komanso zimene tingachite kuti tizilimbikitsa mtendere mumpingo.