Mawu a M'munsi
a Zinthu zonse zabwino zimachokera kwa Yehova. Iye amapereka zinthu zabwino kwa aliyense, ngakhalenso kwa anthu oipa. Koma iye amakonda kuchitira zinthu zabwino makamaka atumiki ake okhulupirika. Munkhaniyi, tiona mmene Yehova amaperekera zinthu zabwino kwa atumiki ake. Tionanso njira yapadera yosonyeza mmene Yehova amaperekera zinthu zabwino kwa atumiki ake amene amasankha kuchita zambiri pomutumikira.