Mawu a M'munsi
a Zimakhalatu zokhumudwitsa kwambiri munthu amene timamukonda akasiya kutumikira Yehova. Nkhaniyi ifotokoza mmene Mulungu amamvera zimenezi zikachitika. Ifotokozanso zimene achibale okhulupirika angachite kuti apirire ululu umene umakhalapo n’kupitiriza kukhalabe olimba mwauzimu. Tionanso zimene onse mumpingo angachite kuti azilimbikitsa komanso kuthandiza achibale a munthu amene wasiya kutumikira Yehova.