Mawu a M'munsi
a Timasangalala anthu akamafuna kumvetsera uthenga wabwino, koma timakhumudwa ngati sakutero. Koma bwanji ngati munthu amene mukuphunzira naye Baibulo sakupita patsogolo? Kapena bwanji ngati simunathandizepo winawake mpaka kufika pobatizidwa? Kodi muyenera kuganiza kuti mwalephera pa ntchito yophunzitsa anthu? Munkhaniyi, tiona zimene tingachite kuti tizichita zambiri mu utumiki n’kumasangalala kaya anthu akumvetsera kapena ayi.