Mawu a M'munsi
a Pamene Yesu ananena kuti nkhosa zake zidzamva mawu ake, ankatanthauza kuti ophunzira ake azidzamvera zimene iye anaphunzitsa n’kumazigwiritsa ntchito pa moyo wawo. Munkhaniyi tikambirana mfundo ziwiri zimene Yesu anaphunzitsa, zomwe ndi kusiya kuda nkhawa kuti tipeza bwanji zofunika komanso kusiya kuweruza ena. Tiona zimene tingachite kuti tizitsatira malangizo akewa.