Mawu a M'munsi
a Lemba la chaka cha 2022, lachokera pa Salimo 34:10. Lembali limati: “Ofunafuna Yehova sadzasowa chilichonse chabwino.” Atumiki ambiri a Yehova alibe katundu kapena ndalama zambiri. Ndiye n’chifukwa chiyani tingati iwo ‘sasowa chilichonse chabwino’? Nanga kodi kumvetsa tanthauzo la vesi limeneli kungatithandize bwanji kukonzekera mavuto amene tingakumane nawo m’tsogolo?