Mawu a M'munsi
a Yehova ndi mnzathu wapamtima. Timaona kuti ubwenzi wathu ndi iye ndi wamtengo wapatali ndipo timafunitsitsa kuti timudziwe bwino. Pamatenga nthawi yaitali kuti tidziwane bwino ndi winawake. Choncho pangafunike nthawi yokwanira kuti tipitirize kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Popeza kuti masiku ano timakhala otanganidwa kwambiri, kodi tingatani kuti tizipeza nthawi yolimbitsa ubwenzi wathu ndi Atate wathu wakumwamba? Nanga kuchita zimenezi kungatithandize bwanji?