Mawu a M'munsi
b MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Dan, yemwe ndi m’bale wachinyamata akuona zimene akulu awiri achita pobwera kudzaona bambo ake kuchipatala. Iye wakhudzidwa kwambiri ndi chikondi chimene akuluwo asonyeza. Nayenso akukhala tcheru kuti azithandiza ena mumpingo. M’bale wina wachinyamata dzina lake Ben, akuona zimene Dan akuchita posonyeza kuganizira ena. Chitsanzo cha Dan chikulimbikitsa Ben kuti athandize pantchito yokonza Nyumba ya Ufumu.