Mawu a M'munsi
a Yehova anatipatsa mphatso yamtengo wapatali yakulankhula. Koma n’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri sagwiritsa ntchito mphatsoyi ngati mmene Yehova ankafunira. Ndiye n’chiyani chingatithandize kuti tizilankhula zoyenera komanso zolimbikitsa m’dziko loipali? Kodi tingatani kuti zolankhula zathu zizisangalatsa Yehova tikakhala mu utumiki, pamisonkhano komanso tikamacheza ndi anthu ena? Munkhaniyi tikambirana mayankho a mafunso amenewa.