Mawu a M'munsi
e MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: John akugwira ovatayimu. Sakufuna kukhumudwitsa abwana ake. Nthawi zonse amavomera abwana ake akamupempha kuti agwire ovatayimu. Madzulo omwewo Tom, yemwe ndi mtumiki wothandiza, wapita ndi mkulu wina ku ulendo wa ubusa. Nthawi ina m’mbuyomu Tom anapempha abwana ake kuti masiku ena mkati mwa mlungu, aziweluka mofulumira kuti azikachita zinthu zina zokhudza kulambira Yehova