Mawu a M'munsi
a Tikamaganizira za munthu yemwe anapirira mayesero aakulu, nthawi zambiri timaganizira za Yobu. Kodi timaphunzira chiyani pa zimene zinamuchitikira? Timaphunzira kuti Satana sangatikakamize kusiya kutumikira Yehova, komanso kuti Yehovayo amadziwa chilichonse chomwe chikutichitikira. Ndipo mofanana ndi mmene anathetsera mavuto a Yobu, tsiku lina adzathetsanso mavuto athu onse. Zochita zathu zikamasonyeza kuti timakhulupirira kwambiri mfundozi, timakhala m’gulu la anthu omwe ‘amayembekezera Yehova.’