Mawu a M'munsi
a Nkhaniyi ifotokoza kamvedwe kathu katsopano kokhudza ntchito yaikulu yophunzitsa yofotokozedwa pa Danieli 12:2, 3. Tiona nthawi yomwe ntchitoyi idzagwiridwe komanso amene adzaigwire. Tionanso mmene ntchito yophunzitsayi idzathandizire anthu okhala padzikoli kukonzekera mayesero omaliza kumapeto kwa Ulamuliro wa Khristu wa Zaka 1,000.