Mawu a M'munsi
b N’kutheka kuti kuukitsidwaku kudzayamba ndi anthu omwe akumwalira ali okhulupirika m’masiku otsiriza ano, n’kumabwerera m’mbuyo m’badwo ndi m’badwo. Ngati umu ndi mmene zidzakhalire, ndiye kuti m’badwo uliwonse udzakhala ndi mwayi wolandira anthu oukitsidwa omwe ankadziwana nawo. Kaya zinthu zidzakhala bwanji, Malemba amafotokoza kuti kuukitsidwa kwa anthu omwe adzapite kumwamba, kudzachitika mwadongosolo kapena kuti “aliyense pamalo pake.” Choncho tinganenenso kuti kuukitsidwa kwa anthu omwe adzakhale padzikoli kudzachitikanso chimodzimodzi.—1 Akor. 14:33; 15:23.