Mawu a M'munsi
a Nzeru zimene Yehova amapereka n’zapamwamba kwambiri kuposa chilichonse chimene dzikoli lingatipatse. Munkhaniyi tiona mawu ochititsa chidwi amene agwiritsidwa ntchito m’buku la Miyambo onena za nzeru yomwe ikufuula m’mabwalo a mzinda. Tikambirana mmene tingapezere nzeru yeniyeni, chifukwa chake ena amakana kumvetsera nzeru yochokera kwa Mulungu komanso mmene timapindulira tikaitsatira.