Mawu a M'munsi
a MATANTHAUZO A MAWU ENA: “Mzimu” wotchulidwa pa Mateyu 26:41, ndi mphamvu yomwe imakhala mkati mwathu, imene imachititsa kuti tizimva kapena kuchita zinthu m’njira inayake. Mawu akuti “thupi” akutanthauza kuti si ife angwiro. Choncho tingakhale ndi zolinga zoyenera zoti tizichita zabwino, koma ngati sitingasamale tingathe kugonja tikayesedwa kuti tichite zimene Baibulo limanena kuti ndi zoipa.