Mawu a M'munsi
a Mabuku a Uthenga Wabwino komanso mabuku ena a m’Baibulo amafotokoza nthawi zingapo pomwe Yesu yemwe anali ataukitsidwa anaonekera kwa anthu monga Mariya wa ku Magadala (Yoh. 20:11-18); amayi ena (Mat. 28:8-10; Luka 24:8-11); ophunzira awiri (Luka 24:13-15); kwa Petulo (Luka 24:34); ophunzira onse kupatulapo Tomasi (Yoh. 20:19-24); ophunzira onse kuphatikizapo Tomasi (Yoh. 20:26); ophunzira 7 (Yoh. 21:1, 2); ophunzira oposa 500 (Mat. 28:16; 1 Akor. 15:6); m’bale wake Yakobo (1 Akor. 15:7); atumwi onse (Mac. 1:4); komanso kwa atumwi pafupi ndi ku Betaniya. (Luka 24:50-52) N’kuthekanso kuti pali maulendo ena omwe anaonekera koma sanalembedwe.—Yoh. 21:25.