Mawu a M'munsi
e Ulosi umenewu uli m’buku la Zekariya ngakhale kuti Mateyu amene analemba nawo Baibulo ananena kuti ulosiwu unanenedwa “kudzera mwa mneneri Yeremiya.” (Mateyu 27:9) Zikuoneka kuti nthawi ina m’mbuyomo buku la Yeremiya, linkaikidwa koyambirira m’mabuku omwe ankadziwika kuti “Zolemba za Aneneri.” (Luka 24:44) Choncho n’kutheka kuti Mateyu ananena kuti ulosiwu uli m’buku la “Yeremiya” pofotokoza za mabuku onse a aneneriwo omwe ankaphatikizaponso buku la Zekariya.