Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
Tulukani
Lowani
Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
Chilengezo
Chinenero chatsopano chomwe chilipo: Dendi
  • Lero

Lamlungu, July 20

Maganizo anga ndi osiyana ndi maganizo anu.​—Yes. 55:8.

Ngati zimene tapempha sizikuchitika tiyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi zimene ndikupemphazi ndi zoyenera?’ Nthawi zambiri anthu timaganiza kuti timadziwa zomwe ndi zoyenera kwa ifeyo. Koma zomwe timapempha zikhoza kukhala zosathandiza kwenikweni. Tikamapempherera vuto linalake, pakhoza kukhala njira ina yabwino yothetsera vutolo kusiyana ndi imene tikupempha. Ndipo zinthu zina zomwe tingapemphe zingakhale zosagwirizana ndi zimene Yehova amafuna. (1 Yoh. 5:14) Mwachitsanzo, taganizirani za makolo omwe anapempha Yehova kuti mwana wawo apitirizebe kukhala m’choonadi. Zimene anapemphazi zikhoza kuoneka ngati zoyenera. Koma Yehova sakakamiza munthu aliyense kuti azimutumikira. Amafuna kuti aliyense azisankha kumutumikira, ngakhalenso ana. (Deut. 10:12, 13; 30:19, 20) M’malomwake makolowo angapemphe Yehova kuti awathandize kuti azimufika pamtima mwanayo n’cholinga choti azikonda Yehova komanso kukhala naye pa ubwenzi.—Miy. 22:6; Aef. 6:4. w23.11 49:5, 12

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lolemba, July 21

Pitirizani kulimbikitsana.​—1 Ates. 4:18.

N’chifukwa chiyani kutonthoza ena kumasonyeza kuti tili ndi chikondi? Buku lina lofotokoza mawu a m’Baibulo linanena kuti mawu akuti “kutonthoza” omwe Paulo anagwiritsa ntchito amatanthauza “kuima pafupi ndi munthu kuti timulimbikitse pamene wakumana ndi vuto lalikulu.” Choncho tikatonthoza m’Khristu mnzathu yemwe wakumana ndi vuto, timamuthandiza kuti aimirire n’kupitiriza kuyenda panjira yokalandira moyo. Nthawi iliyonse yomwe tatonthoza m’bale kapena mlongo, timasonyeza kuti timakonda Akhristu anzathu. (2 Akor. 7:6, 7, 13) Kutonthoza ena n’kogwirizananso ndi chifundo. N’chifukwa chiyani tikutero? Mtima wachifundo ndi umene umalimbikitsa munthu kuti atonthoze ena komanso kuwathandiza. Choncho timayamba ndi kukhala ndi chifundo, kenako timatonthoza ena. Paulo anagwirizanitsa chifundo cha Yehova ndi zimene amachita potonthoza ena. Iye ananena kuti Yehova ndi “Bambo wachifundo chachikulu ndiponso Mulungu amene amatitonthoza pa vuto lililonse.”—2 Akor. 1:3. w23.11 47:8-10

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lachiwiri, July 22

Tikhozanso kumasangalala tikakumana ndi mavuto.—Aroma 5:3.

Otsatira onse a Khristu amayembekezera kukumana ndi mavuto. Taganizirani zimene zinachitikira mtumwi Paulo. Polembera Akhristu a ku Tesalonika, iye anati: “Pamene tinali nanu limodzi, tinkakuuziranitu kuti tidzakumana ndi mavuto ndipo monga mmene mukudziwira, zimene tinkakuuzanizo ndi zimene zachitikadi.” (1 Ates. 3:4) Ndipo kwa Akhristu a ku Korinto, iye analemba kuti: “Abale, tikufuna muzidziwa za mavuto amene tinakumana nawo, . . . tinalibe chiyembekezo choti tikhala ndi moyo.” (2 Akor. 1:8; 11:23-27) Masiku anonso Akhristu angakumane ndi mavuto enaake. (2 Tim. 3:12) Nanga bwanji inuyo? Kodi mwakumana ndi mavuto chifukwa chokhulupirira komanso kutsatira Yesu? Mwina mumanyozedwa ndi anzanu kapena achibale. Mwinanso amakuchitirani nkhanza. Kodi mumakumana ndi mavuto kuntchito chifukwa choyesetsa kuchita zinthu moona mtima? (Aheb. 13:18) Kodi mumatsutsidwa ndi akuluakulu a boma chifukwa chouza ena za chiyembekezo chanu? Kaya tikumane ndi mavuto otani, Paulo anati tiyenera kukhalabe osangalala. w23.12 51:9-10

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • tumizirani
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • zachinsinsi
  • JW.ORG
  • Lowani
tumizirani