NYIMBO 65
Pita Patsogolo
zosindikizidwa
1. Pita patsogolo khala wolimba.
Onetsa kuwala anthu onse aone.
Usonyeze luso muutumiki,
M’lungu akuthandiza.
Utumikiwu ndi wa tonse,
Yesu naye anauchita.
Dalira Mulungu kuti usagwe
Ukhalebe wolimba.
2. Pita patsogolo molimba mtima.
Uzilalikira kwa munthu aliyense.
Tamanda Yehova Mfumu yathuyo
Polalikira nawo.
Adani angakuopseze
Usasiye kulalikira.
Ufumu wa Mulungu wayambadi,
Ulengeze kwa onse.
3. Pita patsogolo usabwerere.
Wonjezera luso ntchito ndi yaikulu.
Mzimu wa Mulungu
ukuthandize,
Udzapeza chimwemwe.
Konda anthu omwe wapeza.
Aphunzitse mogwira mtima.
Athandize kupita patsogolo,
Choonadi chiwale.
(Onaninso Afil. 1:27; 3:16; Aheb. 10:39.)