NYIMBO 115
Tiziyamikira Kuleza Mtima kwa Mulungu
zosindikizidwa
1. Yehova wamphamvu zosatha,
Mumakondatu zabwino.
Zoipa n’zambiri m’dziko,
Mumadziwa n’zosautsa.
Simukuchedwa tikudziwa;
Posachedwa mudzazichotsa.
(KOLASI)
Tiyembekeza mwachidwi,
Timatamanda dzina lanu.
2. Zaka chikwi zilitu ngati,
Tsiku limodzi kwa inu.
Tsiku lanu lalikulu;
Layandikira kwambiri.
Anthu ochimwa akalapa,
Mumasangalala kwambiri.
(KOLASI)
Tiyembekeza mwachidwi,
Timatamanda dzina lanu.
(Onaninso Neh. 9:30; Luka 15:7; 2 Pet. 3:8, 9.)