NYIMBO 11
Chilengedwe Chimatamanda Mulungu
zosindikizidwa
1. Yehova ntchito zanu n’zambiri,
Zakumwamba zitamanda inu.
Chilengedwe chinena za inu;
Ngakhale sichitulutsa mawu.
Chilengedwe chinena za inu;
Ngakhale sichitulutsa mawu.
2. Nzeru yeniyeni ndi yabwino,
Imateteza okuopani.
Mfundo zanu zoposa golide—
N’zothandiza ana ndi akulu.
Mfundo zanu zoposa golide—
N’zothandiza ana ndi akulu.
3. Kudziwa inu n’kothandizadi,
Mawu anu, amapatsa moyo.
Oyeretsa dzina lanu onse,
Mudzawapatsatu madalitso.
Oyeretsa dzina lanu onse,
Mudzawapatsatu madalitso.
(Onaninso Sal. 12:6; 89:7; 144:3; Aroma 1:20.)