NYIMBO 85
Landiranani
zosindikizidwa
1. Takulandirani inu nonse
Mwasonkhana kuti m’phunzire.
Cho’nadi M’lungu amatipatsa;
Timavomera akamatiitana.
2. Tikuyamikira abalewa
Chifukwa amatilandira.
Ndi amenewa tizikondana,
Tilandirenso ena odzasonkhana.
3. Aliyense akuitanidwa,
Ndi M’lungu kudzaphunzitsidwa.
M’lungu watikokera kwa Iye.
Choncho landiranani ndi mtima wonse.
(Onaninso Yoh. 6:44; Afil. 2:29; Chiv. 22:17.)