NYIMBO 77
Kuwala M’dziko Lamdima
zosindikizidwa
1. M’dzikoli mulitu mdima.
Anthu sakumvera.
Kuwala kwatifikira
Ngati m’bandakucha.
(KOLASI)
Uthenga wa M’lungu
Wawala ngati dzuwa
M’dziko lamdimali.
Ukupatsa anthu
Onse chiyembekezo.
Mdima watha.
2. Tidzutse omwe agona
Poti nthawi yatha.
Komanso tiwathandize
Tiwapempherere.
(KOLASI)
Uthenga wa M’lungu
Wawala ngati dzuwa
M’dziko lamdimali.
Ukupatsa anthu
Onse chiyembekezo.
Mdima watha.
(Onaninso Yoh. 3:19; 8:12; Aroma 13:11, 12; 1 Pet. 2:9.)